D.1 Nkhalango
Nkhalango ndi zofunika kuti zizibwezeretsa chinyontho mu mlengalenga kudzera mu nthunzi yomwe imapanga mvula komanso kulimbitsa nthaka pozika mitsitsi m’nthakayo; m’nkhalango mumakhalanso zinthu zamoyo zambiri ndi kusunganso carbon. Ndondomeko iyi ikufotokoza mfundo ndi njira zabwino zosamalira nkhalango achilengewe ndi zochita kubzala zomwe, zobwezeretsa nkhalango m’malo momwe nkhalangozo zatha kuphatikizapo kasankhidwe ka mitengo yaphindu.