A.5 Kusamalira malo okumbika komanso kukola nyansi za m’madzi

Kukokoloka kwa nthaka kumasintha malo otsetsereka kukhala ngalande kapena okumbika ndipo malo olima amachepa. Njira zopewera kukoloka kwa nthaka ndi zomwe zingathandize kuthana ndi kukumbika kwa malo. Malo okumbika akuyenera kukonzedwanso kuopa kuonongeka kwambiri kwa malowo ndi kuguga kwa nthaka. Ndondomekozi zimathandizira popewa kukumbika kwa malo ndi kakonzedwenso ka malo okumbika m’malo okwera/m’minda ndi m’mbali mwa misewu momwe.