A.6 Kusamalira m’mbali mwa mtsinje

Ndondomekozi zimapereka njira zotukulira kalimbidwe ka m’mbali mwa mtsinje kuti musagumuke.Ndondomekozi zikuperekanso njira zokonzeranso m’mbali mwa mtsinje ndi zomera zomwe sizimafa chisawawa.Izi zingabweretse malo abwino ku nyama za m’tchire komanso kupereka chotchingira chabwino pa mtsinjewo zomwe zingateteze mtsinjewo ku nyansi komanso kupereka madzi abwino.